×
UTHENGA WOONA WA YESU KHRISTU
Chicheŵa / Chinyanja

UTHENGA WOONA WA YESU KHRISTU

Wolemba: Bilal Philips
Mawerengedwe: 877

Kufotokozera

Yesu Khirisitu ndi amene agwirizanitsa zipembedzo ziwiri zomwe ziri ndi wotsatira wochuluka m’dziko lino lapansi, Chikhirisitu ndi Chisilamu. Kafukufuku kofuna kupeza uthenga woona wa Yesu ndi umunthu wake kakuchitika kuchokera pa kugwirizanitsa kumeneku.Pali chiyembekezo chakuti kudzera mkafukufuku koteroka Asilamu pamodzi ndi Akristu adzatha kumvetsa bwino kufunika kwa Yesu ndi uthenga wake. Komatu, ngakhale ziri choncho, kwa ife kuti tiupezedi uthenga woona wa Yesu Khirisitu ndipofunika kuchita kalondolondo wokwanira mu kufufuza kwathu kumeneku. Tisalole phuma kuti litsekereze cholinga chathu ndikutipangitsa khungu mmaso mwathu kuti tilephere kuona choonadi. Tifufuze mfundo zonse modekha mtima mogwirizana ndi maganizo a nzeru, kuti tithe kusiyanitsa pakati pa choonadi ndi chabodza Mulungu Wamphamvu yonse.
Tsitsani PDF

Sikani kuti mutsitse

Tsegulani ulalo uwu pa chipangizo chanu kapena sikani QR code kuti mutsitse buku molunjika.

https://islamic-invitation.com/downloads/true_message_jesus_chichewa.pdf

+