×
UTHENGA WOONA WA YESU KHRISTU
Chicheŵa / Chinyanja

UTHENGA WOONA WA YESU KHRISTU

Author: Bilal Philips
Reads: 877

Description

Yesu Khirisitu ndi amene agwirizanitsa zipembedzo ziwiri zomwe ziri ndi wotsatira wochuluka m’dziko lino lapansi, Chikhirisitu ndi Chisilamu. Kafukufuku kofuna kupeza uthenga woona wa Yesu ndi umunthu wake kakuchitika kuchokera pa kugwirizanitsa kumeneku.Pali chiyembekezo chakuti kudzera mkafukufuku koteroka Asilamu pamodzi ndi Akristu adzatha kumvetsa bwino kufunika kwa Yesu ndi uthenga wake. Komatu, ngakhale ziri choncho, kwa ife kuti tiupezedi uthenga woona wa Yesu Khirisitu ndipofunika kuchita kalondolondo wokwanira mu kufufuza kwathu kumeneku. Tisalole phuma kuti litsekereze cholinga chathu ndikutipangitsa khungu mmaso mwathu kuti tilephere kuona choonadi. Tifufuze mfundo zonse modekha mtima mogwirizana ndi maganizo a nzeru, kuti tithe kusiyanitsa pakati pa choonadi ndi chabodza Mulungu Wamphamvu yonse.
Download PDF

Scan to download

Open this link on your device or scan the QR code to download the book directly.

https://islamic-invitation.com/downloads/true_message_jesus_chichewa.pdf